Channel Avatar

Bakili Muluzi TV @UCzBzZegr-kAZtIErmqU7O_A@youtube.com

107K subscribers - no pronouns :c

WELCOME TO THE HOME OF HISTORY. Explaining the lost history


Bakili Muluzi TV
3 months ago - 267 likes

Joe Biden wamuuza Netanyahu kudzera pa phone.
" Tikupangani support poteteza Israel, koma mukayamba nkhondo ndi Iran sitilowelera."

Russia nayonso yachenjeza America.
"Mukamathandiza Israel pa nkhondo imeneyi, nafenso tithandiza Iran."

Dziwani kuti mayiko awiriwa amakhumbana; mwina nthawi yakwana kuti athibulane. Any mistake ndi World War 3.

Anthu a ku Serbia atapha mwana wa mfumu ku Austria-Hungary, World war 1 inayamba mu 1914.
Adolf Hitler atalanda Poland mu 1939, World war 2 inayamba.

Panonso taona Israel ikuphulitsa embassy ya Iran ku Damasiko mpaka kupha asilikali 6. Iran yakwiya ndi kuyambapo kuphulitsa mabomba. America ndi Russia akusapota mbali zosiyana zimene zikubweretsa chiopsezo cha nkhondo yoopsa.

Bakili Muluzi TV
5 months ago - 328 likes

Breaking News!

Chipani cha DPP chasankha mayi Mary Navitcha kukhala New Leader of Opposition. Izi zikudza potsatira chiletso chimene Dr George Chaponda ali nacho ku bwalo la mirandu.

Bakili Muluzi TV
5 months ago - 142 likes

NKHANI ZOCHITIKA KU GAZA STRIP.

Ku Israel, ayuda ochuluka akuchita zionetsero zokakamiza mtsogoleri wao Benjamin Netanyahu kuti atule pansi udindo. Iwowa sakukondwa ndi mmene nkhondo ikuyendera ku Gaza. Asilikali ambiri aphedwa, ma hostage 130 akusowa komanso boma likulephera kukambirana ndi Hamas kuti lipulumutse anthuwa. Ambiri akufuna nkhondoyi ithe ndipo akukakamiza Netanyahu kuti atule pansi udindo.

Nawonso akuluakulu a Hamas ayamba kusemphana mawu. Ismail Haniyeh amene amakhalira ku Qatar, akufuna Israel ichoke ku Gaza ndi kuthetseratu nkhondoyi; Yahya Sinwar amene ali pa ground ku Gaza, akufuna Israel isachoke komanso nkhondo isathe. Iyeyu wapempha kuti pakhale ceasefire ya 6 weeks kenaka ayambirenso nkhondo. Cholinga chake akufuna re-grouping ya Hamas.

Ngakhale asilikali a Israel amaphulitsa mabomba oopsa kwa miyezi itatu ku Gaza, zikuoneka kuti Hamas simatekeseka chifukwa asilikali awo adakalipo ochuluka. Masiku apitawa, pamene Israel inapanga withdraw ku northern Gaza, taona Hamas ikutulukira ndi kumanga maziko kuderalo mpaka atsegula ofesi yawo yokhazikika; apolisi awo abwelera, ma civil servant ayambiranso kugwira ntchito komanso akupatsidwa salary kuchokera kwa Yahya Sinwar.

Bakili Muluzi TV
5 months ago - 214 likes

Dzulo Harry Mkandawire, nduna ya Chakwera, anauza amalawi kuti boma silinalipire bambo Zuneth Sattar. Koma potengera chikalata chimene chapangidwa leak lero, Chakwera anamulipira Sattar ndalama zoposa 8 billion kwacha mmwezi wa November 2023.

Malawi is Not Safe under President Chakwera

Bakili Muluzi TV
5 months ago - 141 likes

Dzulo Gentile Giramata, msilikali wa ku Rwanda amene anapha munthu ku Lilongwe, anakaonekera ku khothi. Talandira malipoti kuti a boma alandira kale chithumba cha ndalama ndipo akuyembekeza kumpatsa bail pa 13 February.

Iyeyu atapha munthu, anathawitsidwa ndi njonda zina za m'boma kudzera pa Mchinji boarder. Koma apolisi a ku Zambia anamugwira pa airport mmwezi wa September chaka chatha pamene amafuna kuthawira ku United States. Anampereka ku Malawi kumene akumusunga kundende.
Mlandu wake wakhala ukuyenda mwansinsinsi chifukwa a boma anadya ndalama za ku Rwanda. Amaletsa ma wayilesi ambiri kulengeza nkhani imeneyi chifukwa akukonza ma plan ofuna kumuthawitsa mu njira ya deportation.

Pamene timafotokoza nkhani imeneyi pa 12 October 2023, ena amayesa nthabwala. Lero ma umboni ayamba kuoneka.
https://youtu.be/JOP7X5EjyoU?si=iYbpV...

Bakili Muluzi TV
5 months ago - 190 likes

Dr Saulos Chilima ndi ololedwa kuyima pa chisankho cha 2025 ngati presidential candidate?

Malemu Justin Malewezi anakhala vice president kwa zaka 10 (1994 mpaka 2004). Koma pa chisankho cha 2004 analoledwa kupikisana nawo ngati presidential candidate.

Pa chisankho cha 2009, malamulo anasinthidwa pamene khothi lidaletsa Dr Bakili Muluzi kupikisana nawo ngati president wa UDF. Ma Judge atatu, Mtambo, Twea ndi Potani, anatsindika kunena kuti president komanso vice president amene wakhala ma term awiri ndi osaloledwa kupikisana nawo pa chisankho potengera ndi malamulo atsopano.

Izi zikutanthauza kuti, president komanso vice president amene analamulirapo ma term awiri sangayime mu 2025. Ku Malawi kuno tili ndi Dr Bakili Muluzi komanso Dr Saulos Chilima amene anakhala mmaudindo awo kwa ma term awiri. Potengera ndi lamulo limeneli, onsewa sakuloledwa kuyimira pa chisankho cha 2025. Akuyenera kupanga retire unless otherwise.

Bakili Muluzi TV
6 months ago - 204 likes

Breaking News!

Agalatiya onse achotsedwa mchipani cha DPP kuyambira lero.

Kondwani Nankhumwa, Nicholas Dausi, Grezedar Jeffrey, Cecilia Chadzama komanso Mark Botomani.

Bakili Muluzi TV
6 months ago - 162 likes

1956, mtsamunda wina otchedwa Shepperson, analemba bukhu limene limafotokoza mbiri ya John Chilembwe. Pofika 1968, MCP inaletsa aliyense kupezeka ndi chithunzi cha Chilembwe. Anatumiza anyamata amene anapita ku P.I.M ndi kukalowa mnyumba za anthu komanso kuotcha zithunzi zonse za Chilembwe. Kuonjezera pamenepo, Kamuzu Banda anachita ban bukhu la Mr Shepperson limene limafotokoza mbiri ya John Chilembwe. Kuyambira 1973, aliyense opezeka akuwerenga bukhu limeneli amanjatidwa kapena kuphedwa.

Ku Phalombe pa Migowi trading centre, kunali agogo a Chigamba amene anamuonapo John Chilembwe komanso kucheza naye in real life. Iwowa analinso cousin wa Garnet Kaduya, mmodzi wa ma comrade amene ananyongewa ndi azungu chifukwa chodula mutu wa Jarvis Livingstone.
Tsiku lina mchaka cha 1981, a MBC anawapanga interview agogo Chigamba kuti acheze nawo zokhudza mbiri imeneyi. Pamene program inali mkati kuulutsidwa, Kamuzu analamula kuti iyimitsidwe komanso ipangiwe delete; ndipo a MBC analetsedwa kuti asadzaulutsenso zimenezo moyo wao onse.

Dziwani kuti John Chilembwe anali ndi ana 4; John Chilembe Jnr, Donald, Emma ndi Sylvia. Emma ndi Sylvia anakwatiwa mwachangu ndipo anabereka ana komanso anawo anawapatsa zidzukulu. Mayi awo Aida anamwalira 1922 ndipo Jnr ndi Donald ankaleledwa ndi mtsamunda wa pa Blantyre mission, Mr Alexander Hertherwick.

Mmodzi wa ana amenewa, John Chilembwe Jnr anamwalira pa 3 February 1970 pa chipatala cha Queen Elizabeth ku Blantyre. Maliro ake sanalemekezedwe ndi boma la MCP ndipo anayikidwa ngati galu. Pamene anali moyo amakhala mu umphawi ndipo Kamuzu analamula ma department onse a boma kuti asadzayerekeze kumulemba ntchito mwana ameneyu.

Kumbukirani kuti mnthawi ya Kamuzu kunalibe Chilembwe Day koma anthu amakumbukira Kamuzu Day. MCP imapusitsa amalawi ndi kumayika sewero la John Chilembwe pa 3 March chaka chilichonse.
3 March was not Chilembwe Day, koma ili ndi tsiku limene Kamuzu Banda ndi anzake achina Henry Chipembere anamangidwa nkukatsekeredwa ku Gwero prison mdziko la Zimbabwe mchaka cha 1959. Komanso sewero limene lija sanayikemo mbiri yeniyeni yofunikira; zokhudza ana ake, mmene Chilembwe anafera komanso kumene anayikidwa anazibisa mwaaladala.

M'busa ameneyu anayamba kupezeka pa ndalama ya kwacha 1997 komanso tinayamba kumukumbukira mwa ulemu mnthawi ya ulamuliro wa Bakili Muluzi.

Umenewu ndi umboni onena kuti chipani cha MCP chinkadana kwambiri ndi m'busa John Chilembwe. Lero ndi zomvetsa chisoni kuona akusintha dzina la chipatala kukhala John Chilembwe hospital chikhalirecho analephera kusamalira ana ake ngakhalenso kulemekeza maliro a mwana weniweni wa M'busa ameneyu, John Chilembwe Jnr.

Akuluakulu! tiyeni tizilemekeza munthu ali ndi moyo. Tisakhale ngati mcp imene imakonda kulemekeza munthu akamwalira. Orton Chirwa anamupha okha lero akufuna kumuwakira manda;
Henry Chipembere anamuthamangitsa mpaka anakafera kunja ndi kuyikidwanso komweko; lero akuti akufuna kumanga Henry Chipembere airport.
Yatuta Chisiza anamupha okha mtembo wake nkukapatsira ng'ona; lero amatiuza kuti anali hero.

1968, A MCP anaotcha zithunzi ndi mabukhu a John Chilembwe ku Chiradzulu; masapota ake anamangidwa komanso kuphedwa; mwana wake Jnr anazunzika ndi umphawi; atamwalira a boma sanamulemekeze; Lero zoona angasinthe dzina la chipatala ndi kukhala John Chilembwe hospital? Zitipindulira chani ngati amalawi poti analephera kale kusamalira ana ake pamene anali ndi moyo?

Bakili Muluzi TV
6 months ago - 97 likes

"Kusagwirizana kwa anthu awiri ndi komwe kukupangitsa kuti Ukraine isachite bwino pa nkhondo."
Akutero akuluakulu a boma ku America.

Kuyambira December 2023, zinaululika kuti pali kusagwirizana pakati pa President Zelensiky ndi mkulu wa asilikali, General Valery Zaluzhnyi; mpaka General anavomereza poyera kuti nkhondo sikuyenda bwino ku mbali ya Ukraine.

Bakili Muluzi TV
6 months ago - 175 likes

Zadziwika tsopano kuti America ndi imene ikusakasaka mkulu wa Hamas, Yahya Sinwar.

Pali kagulu ka asilikali a US intelligence kamene kanasankhidwa kuti kagwire ntchitoyi. Iwowa ndi amene aulura kuti Mr Yahya Sinwar akubisala pansi pa nthaka kudera la Khan Younis; akukhala limodzi ndi ma hostage zomwenso zikulepheretsa kuti amuphulitse.

Mwachidule, America yalowelera nawo nkhondo imeneyi pothandiza israel. Akumenyana ndi ma houlthi, mbali ina akupereka zida za nkhondo komanso ali pa ntchito yofuna kupha Mr Yahya Sinwar