Channel Avatar

Malawian Cameras @UCDhMLf1EGzLRALZ-iOYtb5w@youtube.com

7.37K subscribers - no pronouns set

Malawian Cameras ndi Channel Cha Entertainment


Malawian Cameras
8 minutes ago - 0 likes

Apolisi ati akuchitabe kafukufuku pa chimene chadzetsa imfa ya loya wodziwika bwino a Ralph Kasambara amene amwalira dzulo.

Woyankhulira apolisi m'dziko muno a Peter Kalaya wati malemuwa apezeka atamwalira m'chipinda chogona alendo ku Area 47 mu mzinda wa Lilongwe.

"Kafukufuku achitika lero, kotero kuti zonse zikatha tifotokoza bwino bwino. Sitikufuna kupereka uthenga wabodza," Iwo atero.

A Kalaya awonjezera kuti malemuwa adapezeka atamwalira mchipindamo ndipo adalimo wokha panthawiyo.

Ndipo akubanja ati thupi la malemuwa alitengera mu mzinda wa Blantyre ndipo mawa alitengeranso ku Nkhata Bay kumeneko likalowe m'manda.

Izi ndi malinga ndi malume wa malemuwa a Savous Kasambara.

Pakadalipano, mtsogoleri wa dziko a Lazarus Chakwera wati dziko lino lataya munthu amene adathandizira pa chitukuko cha dziko maka posula ambiri kukhala maloya.

Wolemba: Isaac Salima

Malawian Cameras
4 hours ago - 7 likes

Sad: R.I.P Ralph Kasambara 🕊

Malawian Cameras
6 days ago - 57 likes

Hope Chisanu RIP

Malawian Cameras
6 days ago - 50 likes

Mtsogoleri wa gulu la Mzika Zokhudzidwa Edward Kambanje wamangidwa

M'tsogoleri wa gulu la Mzika Zokhudzidwa a Edward Kambanje wamangidwa kamba ka kalata yomwe analembera bungwe la ACB kuti lifufuze kapezedwe ka galimoto 20 zomwe nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda anagulira mwana wawo momwe akuti munali siginetcha ya membala wa gululi yemwe pano wakana kuti sanasayinire nawo kalatayi.

Malawian Cameras
1 week ago - 37 likes

For those who know this young preacher is No more RIP@muftiyaks

Malawian Cameras
1 week ago - 13 likes

This is true Doc

Malawian Cameras
1 week ago - 17 likes

Mp Esther Ceilia kathumba wapepha Mtsogoleri wa dziko lino kuti akhale president moyo wake onse

Malawian Cameras
1 week ago - 21 likes

Kunyadira ngongole zochoka kwazungu

Malawian Cameras
2 weeks ago - 23 likes

Bwalo la milandu ku Mponela m’boma la Dowa lagamula a Sainani Nkhoma kuti alipire chindapusa cha K200, 000 ponyoza mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.

Koma a Nkhoma akalephera kutero ndekuti akuyenera kukakhala ku ndende miyezi isanu ndi umodzi (6).

Sabata ziwiri zapitazo, a Nkhoma akuti anaponya kanema wonyazitsa a Chakwera pa tsamba la mchezo la WhatsApp lotchedwa Mponera Hotspot.

Woweluza milandu, a Talakwanji M’ndala wati wapereka chigamulochi kuti anthu ena atengerepo phunziro.

Pakadali pano, a Nkhoma ndi mfulu kutsatira kulipira chindapusa chomwe bwaloli linamula.

Wolemba: Mphatso M'bang'ombe

Malawian Cameras
2 weeks ago - 17 likes

Banki yaikulu ya Reserve yatsutsa malipoti oti ikufuna kutsitsa mphamvu ya ndalama ya kwacha ndi 30 percent kumathero a mwezi uno.

Mneneri wa bankiyi, Dr. Mark Lungu, ati omwe akufalitsa nkhaniyi ndi anthu ena omwe akuti ndi osafunira dziko lino zabwino.

Koma katswiri pa chuma, a Christopher Mbukwa, achenjeza kuti kutsitsanso mphamvu kwa ndalamayi kuchititsa kuti mitengo ya katundu ikwere kwambiri komanso ziika aMalawi ambiri pa umphawi wa dzaoneni.

(by Luka Beston-Thyolo:05/22/24)

#malawismostfollowedpage